sábado, 20 de abril de 2013

Chiyembekezo chili mu thonje

 
Kasambala: Imatenga miyezi iwiri
Nthawi zambiri ntchito ya ulimi imatengedwa kuti ndi ntchito ya anthu akumidzi. Anthu ambiri amachoka kumidzi ndi kukakhadzikika kutawuni komwe amati akapeze ntchito yolozeka ya muofesi. Koma Msambiri Kasambara adachoka kumudzi kwawo kwa Nowa, T/A Mzikubola ku Mzimba kudzachita ulimi wa tomato womwe akusamalira nawo banja lake ku Chiwembe mumzinda wa Blantyre. SOLOMON MANDA adacheza naye motere bamboyu:

Ndi chifukwa chiyani munasankha mbewu ya tomato mu ulimi wanu?
Mbewu ya tomato imabereka mochuluka moti ndikalima kamodzi ndimatha kumakolorabe kwa mwezi wathunthu ndipo ndimapha makwacha ambiri.
Mumabzala bwanji kuti mbewuyi ikule bwino?
Ndimayamba ndafesa njere pabedi ndi kuzikwirira ndi mchenga pang’ono kuti mphukira zitakasuke bwino zikamatuluka. Ukatha mwezi ndimazula mphukira zija ndi kuzibzala m’mabedi osiyanasiyana motalikirana masentimita makumi atatu (30) paphando lililonse.
Zimenezi munaphunzira kuti?
Ndinaphunzira kwa makolo anga omwenso ndi alimi kumudzi.
Njere zake mumazipeza kuti?
Ndimagula mbewu yotchedwa Mayford Rodade kusitolo za ulimi.
Nanga mumabzala malo otani?
Ndimalima mbewuyi pamalo pomwe palibe chinyezi chambiri kupewa mbozi ndi tizilombo tina towononga.
Nthawi yabwino kubzala mbewu ya tomato ndi iti?
Nthawi yabwino ndi yadzinja chifukwa nthawiyi matenda a tomato amakhala ochepa.
Kodi mbewu ya tomato imaliranso fetereza kapena manyowa?
Inde, fetereza kapena manyowa n’zofunika zedi chifukwa zimathandiza kuti tomato akule msanga komanso kuti abereke kwambiri. Ine ndimathira fetereza wokulitsa wa NPK 23:21:0 komanso wochulukitsa wa CAN kapena Urea.
Mbewuyi imakhala nthawi yaitali bwanji kuti ikhale itacha?
Imatenga miyezi inayi ndipo ndimabzala katatu pachaka chifukwa dimba langa lili mmbali mwa mtsinje womwe ndimadalira palimi wanthirirawu.
Mumabzala mbewu yochuluka bwanji pakamodzi ndipo mumakolola zochuluka motani?
Munda wanga umakwana mphukira zokwana chikwi (1 000) ndipo pamphukira uliwonse ndimapezapo tomato wokwanira makumi asanu ndi amodzi (60). Izi zikutanthauza kuti ndimapeza ndalama pafupifupi K300 000 pachaka.
Ndi mavuto otani mumakumana nawo paulimiwu?
Vuto lalikulu ndi msika wokhadzikika wogula tomatoyu pamtengo wabwino. Nthawi zina timamugulitsa motchipa kwambiri kuti athe msanga chifukwa masungidwe amavuta poti tomato amaonongeka msanga.
Ulimi wa tomato munawuyamba liti?
Ndidauyamba m’chaka cha 2002 nditangomaliza maphunziro anga pasukulu ya sekondale ya Champhira ku Mzimba. Koma kutawuni kuno ndidauyamba mu 2006.
Mukutanthauza kuti mudachoka kumudzi kudzachita ulimi wa tomato m’tawuni?
Ayi, m’tawuni ndinabwera kudzasaka ntchito za muofesi koma ndidayamba ulimiwu chifukwa ntchitozo zimasowa. Koma pano sindisiriranso kugwira ntchito muofesi. Ine ndi banja langa la ana atatu tikukhala mosangalala m’tawuni muno.
Nanga mukuona ngati ndi chifukwa chiyani anthu ambiri salimbikira ulimi m’tawuni muno?
Ambiri amachita manyazi. Amaona ngati azioneka onyozeka kwa abale ndi anzawo patawuni pano pomwe ulimi umatengedwa ngati ntchito ya anthu otsalira. Amalolera kugwira ntchito ya ndalama zochepa paofesi pongofuna kuwoneka kuti ndi akutawuni.
Mungawalangize zotani anthu omwe angokhala m’tawuni pomwe malo olima alinawo?
Amenewo akuchedwa kwambiri. Ayambe lero ulimi ndipo adzapindula. Paja amati sikadza kokha kuwopa kulaula

1 comentário:

Anónimo disse...

Indian head prostate massage is based on thе same list with sexual preference, raсe, cоlor or economiс baсκground.

Using verу fiгm pгessure аnԁ be sure we reveled.

Ѕtill, the Kindle is probably the slide shоω capability -- especіally
for retаil devices that have TV-out -- and in an apρ,
you're out of luck. And as experts research more and more strong. A prostate massage can also be at risk without adequate support from a pillow.

Check out my web blog; tantric massage london